Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:52 - Buku Lopatulika

52 Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo padziko lake lonse olasidwa adzabuula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo pa dziko lake lonse olasidwa adzabuula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Koma Chauta akunena kuti, “Ikubwera nthaŵi pamene ndidzalange mafano a ku Babiloni, ndipo kubuula kwa anthu olasidwa kudzamveka m'dziko lake lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake, ndipo mʼdziko lake lonse anthu ovulala adzabuwula.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:52
6 Mawu Ofanana  

Chilala chili pamadzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa.


Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.


Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ake, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwake ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa