Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:47 - Buku Lopatulika

47 Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 “Tsono ikudza nthaŵi pamene ndidzalange mafano a Babiloni. Dziko lonselo lidzachita manyazi. Anthu ake onse ophedwa adzakhala ali ngundangunda pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni; dziko lake lonse lidzachita manyazi ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:47
13 Mawu Ofanana  

ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.


chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala;


Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako kukhala akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?


Koma za mneneri, ndi wansembe, ndi anthu, amene adzati, Katundu wa Yehova, ndidzamlanga munthuyo ndi nyumba yake.


Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.


Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala mu Kasidi zoipa zao zonse anazichita mu Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.


Mizinda yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense.


Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo padziko lake lonse olasidwa adzabuula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa