Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo Ine ndiweruza Beli mu Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo Ine ndiweruza Beli m'Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Ndidzalanga Beli, mulungu wa Ababiloni, ndidzamsanzitsa zimene adameza. Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye. Malinga a Babiloni agwa!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni, ndidzamusanzitsa zimene anameza. Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye. Malinga a Babuloni agwa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:44
24 Mawu Ofanana  

Nebukadinezara anatenganso ndi zipangizo za nyumba ya Yehova kunka nazo ku Babiloni, naziika mu Kachisi wake ku Babiloni.


Anachimeza chuma koma adzachisanzanso; Mulungu adzachitulutsa m'mimba mwake.


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.


Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.


Mumfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ake agwa; makoma ake agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; mumbwezere chilango; monga iye wachita mumchitire iye momwemo.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.


Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.


Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.


Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.


Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babiloni adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zake zazitali zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira ntchito chabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.


Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala padziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu.


ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.


ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.


Kumasulira kwake kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha.


Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa