Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:41 - Buku Lopatulika

41 Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 “Ndithu Babiloni wagonjetsedwa, mzinda umene dziko lonse lapansi linkaunyadira walandidwa. Ogo! Babiloni uja wasanduka chinthu chonyansa pakati pa mitundu ya anthu!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 “Ndithu Babuloni walandidwa, mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa! Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ya anthu!

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:41
15 Mawu Ofanana  

Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yehova anatero ndi dziko lino ndi nyumba ino chifukwa ninji?


Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.


pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!


ndi mafumu onse a kumpoto, a kutali ndi a kufupi, wina ndi mnzake; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.


Alekeranji kusiya mzinda wa chilemekezo, mzinda wa chikondwero changa?


Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu!


Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babiloni, ndipo mfuu wamveka mwa amitundu.


Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.


Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri, zikhululuka nkhope zao.


ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.


ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.


Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?


Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa