Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:40 - Buku Lopatulika

40 Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Ndidzapita nawo kuti akaphedwe ngati anaankhosa, ngati nkhosa zamphongo kapena atonde,” akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 “Ine ndidzawatenga kuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa, ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:40
6 Mawu Ofanana  

Pakuti oipa adzatayika, ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa; adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.


Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse; tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.


Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.


Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'mizinda yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.


Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.


Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa anaankhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa