Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:34 - Buku Lopatulika

34 Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, watiwononga, Watitswanya ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ng'ona. Wakhuta ndi zakudya zathu zotsekemera, kenaka nkutilavula.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga, watiphwanya, ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ngʼona, wakhuta ndi zakudya zathu zokoma, kenaka nʼkutilavula.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:34
21 Mawu Ofanana  

Anachimeza chuma koma adzachisanzanso; Mulungu adzachitulutsa m'mimba mwake.


Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu; mudaswa mitu ya zoopsa za m'madzi.


tiwameze ali ndi moyo ngati manda, ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;


Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khwangwala adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.


Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Ndipo Ine ndiweruza Beli mu Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.


Monga Babiloni wagwetsa ophedwa a Israele, momwemo pa Babiloni padzagwa ophedwa a dziko lonse.


Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!


Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.


chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa cha amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;


Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.


Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti,


Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa