Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:30 - Buku Lopatulika

30 Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Ankhondo a ku Babiloni aleka kuponya nkhondo, angokhala khale m'malinga ao. Mphamvu zao zatha, asanduka ngati akazi. Nyumba zake zatenthedwa, mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo; iwo angokhala mʼmalinga awo. Mphamvu zawo zatheratu; ndipo akhala ngati akazi. Malo ake wokhala atenthedwa; mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:30
16 Mawu Ofanana  

Popeza adaswa zitseko zamkuwa, nathyola mipiringidzo yachitsulo.


Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu: Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.


Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao; amuna onse amphamvu asowa manja ao.


Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.


Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.


Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Mumfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ake agwa; makoma ake agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; mumbwezere chilango; monga iye wachita mumchitire iye momwemo.


pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.


Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Zipata zake zalowa pansi; waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake; mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo; inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.


Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.


Taona, anthu ako m'kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako.


chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa