Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo sadzachotsa pa iwe mwala wa pangodya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo sadzachotsa pa iwe mwala wa pangodya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Palibe mwala wako ndi umodzi womwe umene adzabwere nawo kuti augwiritse ntchito ngati mwala wapangodya. Iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,” akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutenga kuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba, chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:26
10 Mawu Ofanana  

Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi maiwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chionongeko, ati Yehova wa makamu.


Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.


Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo.


Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.


Mizinda yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa