Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:16 - Buku Lopatulika

16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m'nyumba za chuma zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m'nyumba za chuma zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba. Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:16
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;


ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula, kapena kulichitira chifundo.


Kodi unalowa m'zosungiramo chipale chofewa? Kapena unapenya zosungiramo matalala,


Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu? Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?


Pa kudzudzula kwanu anathawa; anathawa msanga liu la bingu lanu;


Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.


Atumiza mau ake nazisungunula; aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake.


Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.


Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka, ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.


Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.


Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake.


Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.


Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.


Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.


Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.


Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?


Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.


Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa