Yeremiya 50:9 - Buku Lopatulika9 Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Ndidzasankha ndi kubwera nalo gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ya anthu lochokera kumpoto, kuti lidzamenyane ndi Babiloni. Mivi yao ili ngati ya wankhondo waluso, yosapita padera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto kudzamenyana ndi Babuloni. Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni. Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso, yosapita padera. Onani mutuwo |