Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 50:41 - Buku Lopatulika

41 Taonani, anthu achokera kumpoto; ndiwo mtundu waukulu, ndipo maufumu ambiri adzaukitsidwa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Taonani, anthu achokera kumpoto; ndiwo mtundu waukulu, ndipo maufumu ambiri adzaukitsidwa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 “Onani, ankhondo akubwera kuchokera kumpoto. Anthu a mtundu wanyonga ndi mafumu ambiri akunyamuka kuchokera ku madera akutali a dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 “Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri, wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 50:41
11 Mawu Ofanana  

Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu aakulu adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa machitidwe ao, monga mwa ntchito ya manja ao.


Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe.


Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Kumasulira kwake kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha.


Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, ndipo zidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, ndi kudya nyama yake, ndipo zidzampsereza ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa