Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 50:4 - Buku Lopatulika

4 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israele adzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m'njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israele adzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m'njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chauta akunena kuti, “Masiku amenewo, nthaŵi imeneyo Aisraele ndi Ayuda adzasonkhana pamodzi, azikabwera nalira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Chauta Mulungu wao afuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 50:4
32 Mawu Ofanana  

ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.


Funani Yehova, ndi mphamvu yake; funsirani nkhope yake nthawi zonse.


Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.


Ine sindinanene m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona.


Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;


Pakuti tsiku lakubwezera lili mumtima mwanga, ndi chaka cha kuombola anthu anga chafika.


Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda;


Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dzikomu.


Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka mu Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu.


Pamenepo udzakumbukira njira zako ndi kuchita manyazi, pakulandira abale ako aakulu ndi aang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako aakazi, angakhale sali a pangano lako.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje.


Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu.


Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa