Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 50:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Mtundu wa anthu akumpoto wadzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Dziko lake adzalisandutsa bwinja, ndipo kumeneko sikudzakhalanso munthu kapena nyama.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babuloni ndi kusandutsa bwinja dziko lake. Kumeneko sikudzakhalanso munthu kapena nyama.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 50:3
22 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.


Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.


Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.


Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:


Ndipo ndidzakantha okhalamo m'mzinda uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi mliri waukulu.


Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe.


Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zili m'menemo, zidzaimba mokondwerera Babiloni; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kuchokera kumpoto, ati Yehova.


nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi.


Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa