Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 5:26 - Buku Lopatulika

26 Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba, amene amalalira anzao monga m'mene amachitira otchera mbalame. Amatcha misampha nakola anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:26
16 Mawu Ofanana  

Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?


Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa;


Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.


Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao?


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa