Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 5:21 - Buku Lopatulika

21 Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 “Imvani izi, inu anthu opusa, opanda ndi nzeru zomwe, inu amene maso muli nawo, koma simupenya, amene makutu muli nawo, koma simumva.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru, inu amene maso muli nawo koma simupenya, amene makutu muli nawo koma simumva.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:21
26 Mawu Ofanana  

Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?


Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la chitsiru, popeza wopusa alibe mtima?


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.


Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Nenani ichi m'nyumba ya Yakobo, lalikirani mu Yuda, kuti,


Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena chiweruzo cha Mulungu wao.


Ndidzanena ndi yani, ndidzachita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao lili losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.


Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamve; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankhe;


Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake; ndipo njiwa ndi namzeze ndi chingalu ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa chiweruziro cha Yehova.


Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.


Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya.


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.


Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi?


Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.


ndi kuti, Pita kwa anthu awa, nuti, Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;


Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;


monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.


mayesero aakuluwa maso anu anawapenya, zizindikirozo, ndi zozizwa zazikulu zija;


koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.


Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa