Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 5:15 - Buku Lopatulika

15 Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 “Iwe Israele, ndikukudzetsera mtundu wa anthu odzakuthira nkhondo, mtundu wake ndi wochokera kutali. Mtundu umenewu ndi wosagonjerapo, mtundu wakalekale, mtundu umene chilankhulo chake iwe suchidziŵa, ndipo zimene akunena, iwe sungazimvetse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Inu Aisraeli,” Yehova akuti, “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali, ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo, mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa, zimene akunena inu simungazimvetse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:15
27 Mawu Ofanana  

Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.


Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.


Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;


Ndipo ndidzamanga zithando kuzungulira iwe ponse, ndipo ndidzamanga linga ndi kuunjika miulu yakumenyanirana ndi iwe.


Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi chivomezi, ndi mkokomo waukulu, kamvulumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.


Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilime lachibwibwi, limene iwe sungalimve.


Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni.


Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutali mbendera, nadzawaimbira mluzu, achokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msangamsanga;


Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.


Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;


taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.


Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera mizinda ya Yuda mau ao.


Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova.


Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.


Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima.


Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.


Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha.


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.


Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa