Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 5:13 - Buku Lopatulika

13 ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mau a aneneri azikangopita ngati mphepo, ndipo uthenga wao si wa kwa Mulungu. Zimene amanena zidzaŵagwera iwo omwewo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo; ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova. Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:13
13 Mawu Ofanana  

koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.


Kodi muyesa kudzudzula mau? Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.


Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?


Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.


Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.


Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi chilala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.


Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatume, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa.


Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.


Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa chifukwa cha choipa chako chonse.


Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anazichotsa muno, kunka nazo ku Babiloni;


pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe mu Ejipito kukhala m'menemo;


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa