Yeremiya 49:7 - Buku Lopatulika7 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi m'Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Za Edomu, Chauta Wamphamvuzonse akufunsa kuti, “Kodi nzeru sizikupezekanso ku Tema? Kodi anzeru uphungu wao udatheratu? Kodi nzeru zao zija zati zii? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu: “Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani? Kodi anzeru analeka kupereka uphungu? Kodi nzeru zawo zinatheratu? Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.