Yeremiya 49:5 - Buku Lopatulika5 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Chenjerani, mudzaona zoopsa kuchokera kwa onse okuzungulirani. Adzakupirikitsani muli kaŵeraŵera, popanda wina wokusonkhanitsaninso othaŵanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe zochokera kwa onse amene akuzungulira,” akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse. “Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake. Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo. Onani mutuwo |
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.