Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 49:4 - Buku Lopatulika

4 Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chifukwa chiyani mukunyadira zigwa zanu, inu anthu osakhulupirika, amene munkadalira chuma chanu nkumati, ‘Ndani angalimbane ndi ife?’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Chifukwa chiyani mukunyadira chigwa chanu, inu anthu osakhulupirika amene munadalira chuma chanu nʼkumati: ‘Ndani angandithire nkhondo?’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 49:4
18 Mawu Ofanana  

Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao;


Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.


Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.


Chuma cha wolemera ndi mzinda wake wolimba; koma umphawi wao uononga osauka.


Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?


Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mzinda uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;


Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.


Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.


Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;


Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa