Yeremiya 49:30 - Buku Lopatulika30 Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala mu Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201430 Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa30 Inu anthu a ku Hazori, thaŵani, fulumirani, kabisaleni ku makwaŵa. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, wakonzekera kuti amenyane nanu,” akutero Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero30 “Thawani mofulumira! Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,” akutero Yehova. “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu; wakonzekera zoti alimbane nanu. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.