Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 49:2 - Buku Lopatulika

2 Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo midzi yake idzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ake akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipotu nthaŵi ikudza, pamene ndidzamveketse mfuu wankhondo ku Raba, likulu la ku Amoni. Mzinda umenewo udzasanduka bwinja lopanda anthu, ndipo midzi yake idzapserera. Tsono Israele adzaŵalanda zao adaniwo amene adamulanda zake,” akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo ku Raba, likulu la Amoni; ndipo malo awo opembedzera milungu yawo adzatenthedwa ndi moto. Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 49:2
22 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.


Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana aakazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu.


Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.


Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.


Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mzinda, ndimo udzangokhala muunda wopasulidwa.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'mizinda mwake?


Uiike njira yodzera lupanga kunka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.


Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israele, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza;


koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;


Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi.


Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.


Ndipo Israele analanda mizinda iyi yonse; nakhala Israele m'mizinda yonse ya Aamori; mu Hesiboni ndi midzi yake yonse.


Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mzinda, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.


(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).


Ndipo mu Isakara ndi mu Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.


Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m'dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala mu Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m'chigwa cha Yezireele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa