Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 49:14 - Buku Lopatulika

14 Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ndamva uthenga wochokera kwa Chauta wamthenga watumidwa kwa anthu a mitundu ina. Akufuula kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti mumenyane ndi Edomu, dzambatukani mukonzekere nkhondo!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu! Konzekerani nkhondo!”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 49:14
12 Mawu Ofanana  

Pakuti akalonga ake ali pa Zowani, ndi mithenga yake yafika ku Hanesi.


Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka kudziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.


Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng'ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.


Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.


Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa