Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 “Wothaŵa nkhaŵa, adzagwa m'dzenje. Wotuluka m'dzenje, adzakodwa mu msampha. Zimenezi nzimene ndidzamgwetsere Mowabu pa nthaŵi ya chilango chake,” akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 “Aliyense wothawa zoopsa adzagwera mʼdzenje, aliyense wotuluka mʼdzenje adzakodwa mu msampha. Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu pa nthawi ya chilango chake,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:44
22 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu.


Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mzinda, m'chipinda cha m'katimo.


Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?


Mantha ndi dzenje ndi msampha zili pa iwe, wokhala m'dziko.


Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.


Ndiwo chabe, ndiwo chiphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha.


ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera choipa pa anthu a ku Anatoti, chaka cha kulangidwa kwao.


Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.


Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.


Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwe, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova.


Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.


Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.


Mantha ndi dzenje zitifikira, ndi phokoso ndi chionongeko.


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.


Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa