Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:26 - Buku Lopatulika

26 Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzamvimvinika m'kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzavimvinika m'kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Mledzeretseni Mowabu chifukwa adadzikuza poukira Chauta. Avimvinizike m'masanzi ake omwe. Akhale chinthu chomachiseka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 “Muledzeretseni Mowabu, chifukwa anadzikuza powukira Yehova. Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake; mulekeni akhale chinthu chomachiseka.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:26
37 Mawu Ofanana  

Pakuti amtambasula dzanja lake moyambana ndi Mulungu, napikisana ndi Wamphamvuyonse.


Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?


Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.


Koma Inu, Yehova, mudzawaseka; mudzalalatira amitundu onse.


Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.


Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.


Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.


Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?


Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.


Yehova wasakaniza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.


Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udyo, palibe malo okonzeka.


Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandidzandi; koma si ndi chakumwa chaukali.


Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova chikho cha ukali wake; iwe wamwa mbale ya chikho chonjenjemeretsa ndi kuchigugudiza.


Ndipo ndinapondereza anthu m'kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao.


Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.


Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.


Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.


Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.


Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.


Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza; adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu; mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula, ndipo iwowo adzanga ine.


Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa chivumulo.


kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako.


Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika.


koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.


Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, ndi kuzipondereza.


Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira chifukwa cha mdani.


Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako.


amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa