Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:18 - Buku Lopatulika

18 Iwe mwana wamkazi wokhala mu Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 “Inu anthu a ku Diboni, tsikanipo pa ulemerero wanu, khalani pansi poumapa. Woononga Mowabu wafika kudzamenyana nanu, wapasula malinga anu ankhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Tsikani pa ulemerero wanu ndipo khalani pansi powuma, inu anthu okhala ku Diboni, pakuti wowononga Mowabu wabwera kudzamenyana nanu, wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:18
13 Mawu Ofanana  

Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira.


Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?


Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.


Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.


Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.


ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu;


Ndipo tsopano waokedwa m'chipululu m'dziko louma ndi la ludzu.


Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba.


Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,


Hesiboni ndi mizinda yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni;


kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;


Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa