Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:14 - Buku Lopatulika

14 Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Kodi mungathe kunena bwanji kuti, ‘Ife ndife ngwazi, asilikali olimba mtima pa nkhondo?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali. Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:14
12 Mawu Ofanana  

Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?


Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa, mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona.


Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.


Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu;


Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.


Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Bwanji muti, Tili ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lachita zonyenga.


Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;


Atero Yehova, Iwonso ochirikiza Ejipito adzagwa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatsika, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene adzagwa m'kati mwake ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.


Ichi adzakhala nacho m'malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa