Yeremiya 48:12 - Buku Lopatulika12 Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Chauta akunena kuti, “Chenjerani tsono, akubwera masiku pamene ndidzatuma anthu oti Mowabuyo adzamkhuthule ngati vinyo. Kenaka mitsuko yake itasanduka yopanda kanthu m'kati, ndidzaiphwanya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Nʼchifukwa chake masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko ndipo adzamukhutula; adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.