Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:11 - Buku Lopatulika

11 Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira unyamata wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina. Sadatengedwe ukapolo. Nchifukwa chake khalidwe lake lili losasinthika, ndipo fungo lake lili lomwe lija.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina; iye sanatengedwepo ukapolo. Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja ndipo fungo lake silinasinthe.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:11
16 Mawu Ofanana  

Moyo wathu wakhuta ndithu ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu, ndi mnyozo wa odzikuza.


Mulungu adzamva, nadzawasautsa, ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, ndipo saopa Mulungu.


Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.


Dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova anenana mau amenewa.


Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.


Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.


Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.


Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.


Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.


Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.


Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa