Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 47:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamzinda ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adati, “Onani m'mene madzi akubwerera kuchokera kumpoto, adzakhala mtsinje wosefukira ndi wamkokomo. Adzasefukira m'dzikomo ndi kumiza zonse zokhala m'menemo, mizinda yonse, ndi anthu onse okhalamo. Anthu azidzafuula, onse okhala m'dzikomo azidzalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova akuti, “Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto; adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo. Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo, mizinda ndi onse okhala mʼmenemo. Anthu adzafuwula; anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 47:2
32 Mawu Ofanana  

Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.


Ndikamva njala, sindidzakuuza, pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.


Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake.


Nyanja ifuule ndi kudzala kwake; dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;


Lira, chipata iwe; fuula, mzinda iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake.


Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.


Katundu wa chigwa cha masomphenya. Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamatsindwi?


Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.


Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Kuchokera kumpoto choipa chidzatulukira onse okhala m'dziko.


Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.


Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.


Ejipito ndi ng'ombe yaikazi yosalala; chionongeko chotuluka kumpoto chafika, chafika.


Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m'manja a anthu a kumpoto.


Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.


Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.


Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.


Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano.


Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima.


pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.


Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.


Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.


Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,


Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa