Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 43:7 - Buku Lopatulika

7 ndipo anadza nalowa m'dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndipo anadza nalowa m'dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Onsewo adapita nawo ku Ejipito monyoza mau a Chauta, nakafika ku Tapanesi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kotero anthuwo analowa mʼdziko la Igupto chifukwa anakana kumvera Yehova, nakafika ku Tapanesi.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 43:7
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo ananyamuka anthu onse aang'ono ndi aakulu, ndi akazembe a makamu, nadza ku Ejipito; pakuti anaopa Ababiloni.


Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


amene ayenda kutsikira ku Ejipito, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito!


Pakuti akalonga ake ali pa Zowani, ndi mithenga yake yafika ku Hanesi.


Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamutu pako.


ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,


Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m'chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.


Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,


Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Ejipito.


Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.


Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa