Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 43:5 - Buku Lopatulika

5 Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, adatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene adabwerera kuchokera ku maiko kumene adaabalalikira kuti akakhale ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mʼmalo mwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo anatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene anabwera kudzakhala mʼdziko la Yuda kuchokera ku mayiko onse kumene anabalakirako.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 43:5
7 Mawu Ofanana  

Koma kunena za anthu otsalira m'dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira.


Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'mizinda imene mwailanda.


Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.


ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,


Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa