Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 43:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo, pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, adakana kumvera Chauta ndipo sadakhale ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Motero Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi anthu onse sanamvere lamulo la Yehova loti akhale mʼdziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 43:4
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo ananyamuka anthu onse aang'ono ndi aakulu, ndi akazembe a makamu, nadza ku Ejipito; pakuti anaopa Ababiloni.


Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.


Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.


Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni;


Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m'chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.


Ndipo anaitana Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu,


Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa