Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 43:3 - Buku Lopatulika

3 koma Baruki mwana wake wa Neriya atisonkhezera zoipa za inu, mutipereke m'dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 koma Baruki mwana wake wa Neriya atichichizira inu, mutipereke m'dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Baruki mwana wa Neriya ndiye wakukakamiza kuti utiletse, ndipo kuti tigwe m'manja mwa Ababiloni, kuti atiphe kapena kutitenga ukapolo kupita ku Babiloni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma ndi Baruki mwana wa Neriya amene akukulimbikitsa kuti utiletse zopita ku Igupto ndi kuti mʼmalo mwake tidzipereke mʼmanja mwa Ababuloni, kuti iwo atiphe kapena kutitenga ukapolo ku Babuloni.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 43:3
12 Mawu Ofanana  

M'malo mwa chikondi changa andibwezera udani; koma ine, kupemphera ndiko.


ndipo ndinapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata yogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse.


Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.


Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m'dzikomo.


ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;


Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa