Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 43:10 - Buku Lopatulika

10 ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono uŵauze kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ndidzaitana mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaika mpando wake pa miyala imene ndaibisa apoyo. Ndipo adzafunyulula hema lake laufumu pa miyalayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayitana mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzakhazika mpando wake waufumu pa miyala imene ndayikwirira apayi. Iye adzafunyulula tenti yake yaufumu pa miyala imeneyi.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 43:10
19 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamzindapo.


Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.


Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga; mdima wa madzi, makongwa a kuthambo.


Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.


Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.


ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.


Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:


Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.


Tenga miyala yaikulu m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao mu Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;


Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.


ndipo ndidzaika mpando wachifumu wanga mu Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.


Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa