Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 43:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yeremiya atatsiriza kuuza anthu zonse zimene Chauta Mulungu wao adamtuma kuti akaŵauze,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yeremiya atatsiriza kuwawuza anthuwo mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova anamutuma kuti akawawuze,

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 43:1
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.


Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.


Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.


Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.


Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa mizinda yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.


Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.


Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m'chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.


Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, komwe mufuna kukakhalako.


Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; choipa sichidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;


Ndipo padzakhala, utatha kuwerenga buku ili, ulimange ndi mwala, nuliponye pakati pa Yufurate;


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.


Ndipo Samuele anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa