Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 42:16 - Buku Lopatulika

16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 ndiye kuti nkhondo mukuiwopayo idzakugonjetsani ku Ejipito komweko. Njala mukuiwopayo idzakuvutanibe ngakhale ku Ejipitoko, ndipo mudzafera kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 ndiye nkhondo imene mukuyiopayo idzakugonjetsani ku Igupto komweko. Njala imene mukuyiopayo idzakupezani ku Igupto komweko ndipo mudzafera kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 42:16
13 Mawu Ofanana  

Zoipa zilondola ochimwa; koma olungama adzalandira mphotho yabwino.


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m'dzikomo.


Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;


Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.


Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.


Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.


Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.


Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa