Yeremiya 41:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Pambuyo pake Ismaele adaŵatenga ukapolo anthu onse amene adatsala ku Mizipa. Anthuwo ndi aŵa: ana aakazi a mfumu, ndi onse otsala ku Mizipa, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa nkhondo adaŵapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wao. Ndipo anthu ameneŵa adachoka nawo ndi cholinga choti akaloŵe nawo m'dziko la Aamoni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni. Onani mutuwo |