Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 4:29 - Buku Lopatulika

29 Mzinda wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; mizinda yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Anthu a m'mudzi uliwonse adzathaŵa, pakumva phokoso la ankhondo okwera pa akavalo ndi oponya mivi. Azikati uku ena akuloŵa m'nkhalango, ena akukwera m'mathanthwe. Mizinda yonse kuisiya, popanda ndi mmodzi yemwe wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi, anthu a mʼmizinda adzathawa. Ena adzabisala ku nkhalango; ena adzakwera mʼmatanthwe mizinda yonse nʼkuyisiya; popanda munthu wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:29
14 Mawu Ofanana  

Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.


Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba paphiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.


ndipo Yehova wasunthira anthu kutali, ndi mabwinja adzachuluka pakati padziko.


Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.


Pamenepo anaboola mzinda, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mzinda usiku panjira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pamunda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mzinda pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha.


Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.


Ndinaona Ambuye alikuima paguwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi.


Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.


Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa