Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 4:26 - Buku Lopatulika

26 Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo mizinda yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo midzi yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Ndidayang'ana, dziko la chonde linali litasanduka chipululu, mizinda yake yonse inali itasanduka mabwinja, chifukwa cha mkwiyo wa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu; mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:26
15 Mawu Ofanana  

Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?


Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri.


Ndipo ndidzaletsa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Ambuye wataya guwa lake la nsembe, malo ake opatulika amnyansira; wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake; iwo anapokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.


Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa