Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 4:19 - Buku Lopatulika

19 Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mayo, mayo, ati kupweteka ati! Ha, mtima wanga ukuŵaŵa, ukugunda moti thithithi. Sindingathe kukhala chete. Ndikumva kulira kwa lipenga ndi mfuu yankhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mayo, mayo, ndikumva kupweteka! Aa, mtima wanga ukupweteka, ukugunda kuti thi, thi, thi. Sindingathe kukhala chete. Pakuti ndamva kulira kwa lipenga; ndamva mfuwu wankhondo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:19
48 Mawu Ofanana  

Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.


Nati kwa atate wake, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amake.


Ndipo anamyang'ana chidwi, mpaka anachita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.


Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.


Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; pakuti Yehova anakuchitira chokoma.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Ndinasumwa kwakukulu, chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.


Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu.


Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.


Chifukwa chake m'mimba mwanga mulirira Mowabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi.


Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.


Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.


Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.


Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?


Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.


ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;


Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo midzi yake idzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.


Phokoso la nkhondo lili m'dziko lino, ndi lakuononga kwakukulu.


Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.


Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandivuta.


Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga.


Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.


Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.


Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.


Pakuti ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?


Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,


Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni. Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa