Yeremiya 39:6 - Buku Lopatulika6 Pamenepo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya ku Ribula pamaso pake; mfumu ya ku Babiloni niphanso aufulu onse a Yuda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Pamenepo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya ku Ribula pamaso pake; mfumu ya ku Babiloni niphanso aufulu onse a Yuda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono mfumu ya ku Babiloni idapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribula, iyeyo akuwona. Idaphanso atsogoleri onse a ku Yuda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ku Ribulako, mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona. Inaphanso anthu olemekezeka onse a ku Yuda. Onani mutuwo |
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.