Yeremiya 39:5 - Buku Lopatulika5 Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola ndi kukamgwira Zedekiyayo ku zigwa za ku Yeriko. Mfumuyo ataigwira, adapita nayo kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ku Ribula m'dziko la Hamati. Ndipo adagamula mlandu wake komweko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake. Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.