Yeremiya 39:16 - Buku Lopatulika16 Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mzinda uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 “Pita ukauze Ebedemeleki Mkusi uja kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akunena kuti, ‘Zidzachitikadi zimene ndidaanena za mzinda uno, ndipo nzoipa osati zabwino, ai. Zidzachitikadi pa nthaŵi yake, iwe ukupenya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 “Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona. Onani mutuwo |