Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 39:12 - Buku Lopatulika

12 Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umchitire monga iye adzanena nawe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umchitira monga iye adzanena nawe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Mtenge, umsamale bwino, usamvute, koma umchitire zimene afuna.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Mutenge, umusamale bwino, ndipo usamuvute koma umuchitire zimene afuna.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:12
12 Mawu Ofanana  

Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.


Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi ya nsautso.


Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.


Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkulu wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Neregali-Sarezere mkulu wa alauli, ndi akulu onse a mfumu ya ku Babiloni;


Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.


Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.


namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa