Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 39:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adatumiza mau kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo, onena za Yeremiya. Adati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Tsono Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inatuma mawu kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu za Yeremiya. Iye anati:

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:11
12 Mawu Ofanana  

Apulumutsa aumphawi kulupanga la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu.


Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo, ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.


Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.


Usaope nkhope zao; chifukwa Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.


Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi ya nsautso.


Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.


Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.


Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ake, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babiloni.


Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.


Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa mu Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:


Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa