Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 39:1 - Buku Lopatulika

1 Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ndi gulu lake lonse lankhondo ku Yerusalemu, nazinga mzindawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:1
16 Mawu Ofanana  

Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,


Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumzinda uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.


Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.


Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.


Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mzinda wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso.


Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri cha undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lachisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mzinda.


Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.


Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mzindawo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa