Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 38:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa Chipata cha Benjamini;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa chipata cha Benjamini;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Ebedemeleki, Mkusi wina wofulidwa wogwira ntchito ku nyumba ya mfumu, adamva kuti Yeremiya amponya m'chitsime. Nthaŵi imeneyo nkuti mfumu ili ku Chipata cha Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:7
22 Mawu Ofanana  

Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.


Akulu adzafumira ku Ejipito; Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.


Anthu ankhanza ada wangwiro; koma oongoka mtima asamalira moyo wake.


Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ake; pena mfule asanene, Taonani ine ndili mtengo wouma.


Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.


Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali mu Chipata cha Benjamini cha kumtunda, chimene chinali kunyumba ya Yehova.


Pamenepo akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m'dzina la Yehova Mulungu wathu.


anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,


akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m'dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwanawang'ombe;


Pokhala iye mu Chipata cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni.


Ebedemeleki anatuluka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,


Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.


Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.


Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.


azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mzinda wake, ndi ku chipata cha malo ake;


Munthu akathawira umodzi wa mizinda iyi, aziima polowera pa chipata cha mzindawo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mzindawo; pamenepo azimlandira kumzinda kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa