Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 38:22 - Buku Lopatulika

22 Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda, adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni. Popita ku Babiloniko, akazi amenewo azidzaimba kuti, “ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja adakunyenga, ndipo adakugonjetsa. Tsopano poti miyendo yako yazama m'matope, abwenzi akowo akusiya.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti, “ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa, ndipo anakugonjetsa. Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope; abwenzi ako aja akusiya.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:22
22 Mawu Ofanana  

Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje, ngati madzi a timitsinje akupitirira.


Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Mundilanditse kuthope, ndisamiremo, ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.


Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo; ndalowa m'madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.


Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.


Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako kukhala akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babiloni; pakuti akunenerani zonama.


Pakuti sindinawatume iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.


Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.


Koma ngati mukana kutuluka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa:


Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.


ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;


Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.


Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.


Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.


Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.


Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Anaipitsa akazi mu Ziyoni, ndi anamwali m'midzi ya Yuda.


Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa