Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 38:18 - Buku Lopatulika

18 koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Koma mukangopanda kudzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'manja mwa Ababiloni, ndipo adzautentha, tsono inu simudzapulumuka m'manja mwao.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:18
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.


Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mzinda uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.


Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Neregali-Sarezare mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.


Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa